Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Mnyamata wazaka 17 wapha mphunzitsi

Apolisi ku Chiradzulu akusunga mnyamata wazaka 17 pomuganizira kuti wabaya ndi mpeni mphunzitsi wazaka 33, Shadreck Banda yemwe wamwalira kuchipatala pomwe mzake wa mphunzitsiyo Wilfred Manyamba, yemwe anamubayanso, amugoneka kuchipatala.

Mneneri wapolisi ku Chiradzulu Cosmas Kagulo wati mphunzitsi ndi mzakeyo anali pasiwa. Ndipo kanthawi kena anachoka pasiwapo kukafufuza mowa kuti amwe achotse tulo.

Koma ali munjira anakumana ndi mnyamatayo yemwe ananyamula thumba momwe munali nkhumba. Atamufunsa, mnyamatayo anathawira mnyumba mwa makolo ake kenako ndikutuluka ndi mpeni ndikubaya awiriwo. Izi zachitika kwa Walala Mfumu yaikulu Likoswe m’boma lomwelo la Chiradzulu.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

T/A Amidu alowa mmanda

MBC Online

Awanjata pogulitsa mankhwala owopsa

Blessings Kanache

Dr Chakwera aona ukadaulo wanga — Chambo

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.