Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Ayamikira Chitukuko cha milatho

Alimi ang’ombe za mkaka mmadera a Satemwa ku Thyolo ndi Mpemba ku Blantyre ati milatho yomwe bungwe la TRADE Programme lamanga mmadera awo ithandiza kuti adzitha kufikira ku malo ogulitsirako mkaka mnyengo zonse.

Malinga ndi wapampando wamalo ogulitsirapo mkaka a Mpeni ku Thyolo, a Clemence Masauli, komwe ena mwa alimi  ake akugwiritsa ntchito mlatho wa Nsuwadzi, mmbuyomu nthawi yamvula alimi amalephera kukagulitsa mkaka kaamba kakusowa kwa mlatho.

Nawonso alimi ang’ombe za mkaka amdera la mfumu Davide ku Mpemba m’boma la Blantyre ati kumangidwa kwa milatho iwiri mderali kwathandiza ulimi wawo.

“Tikuthokoza boma potithandiza kudzera mu bungwe la TRADE Programme, mayendedwe afewa ndithu mdera lino,” anatero mayi Elesi Kalirombe

A TRADE Programme aika padera ndalama zokwana pafupifupi K20 billion mwazina  zomangira milatho ndi misewu kuti alimi adzitha kufikira misika mosavuta. A TRADE Programme akulimbikitsa ntchito yoti alimi adzitenga ulimi ngati bizinesi.

 

Olemba: Geoffrey Chinawa

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

‘Anthu opitilira 3,000 amwalira kaamba ka vuto la mpima’

Lonjezo Msodoka

Kasungu mourns Kapheni

MBC Online

DWF champions training for improved parliamentary performance

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.