Achinyamata m’dziko muno ati mkumano wa pakati pa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera ndi iwo, umene ukuyembekezeka kukhalapo mawa Lachisanu, chikhale chiyambi.
Mkulu wa bungwe la Youth and Society, a Charles Kajoloweka, komanso mtsogoleri wa ophunzira pa sukulu ya Kamuzu University of Health Sciences (KUHeS), a Eric Magetsi, ndi amene anena izi ndipo ayamikira Dr Chakwera kaamba ka chikonzerochi.
A Kajoloweka ati akuyembekezera kumva m’mene mtsogoleriyu wachitira pansi pa ndondomeko ya Youth Manifesto, imene adasayinira asanalowe m’boma.
A Magetsi ati akuyembekezera achinyamata kutula nkhawa zawo pa zamaphunziro, mwayi wa ntchito komanso chitukuko, mwazina.
Mkumanowu, umene uchitikire ku nyumba yaboma munzinda wa Lilongwe, udzakhalanso pa masamba a mchezo a Dr Chakwera pa Facebook ndi pa X.
Mtsogoleri wa dziko linoyu adzatambasula zitukuko zimene adalengeza mu uthenga wa SONA sabata yatha komanso kuyankha mafunso ndi kumva maganizo kuchokera kwa achinyamata.