Katswiri oyimba nyimbo za Amapiano, Temwa, wati iye ndi odzipereka kuthandiza ana osowa amene agonekedwa mu zipatala m’dziko muno.
Temwa amayankhula izi pa chipatala cha Kamuzu Central munzinda wa Lilongwe pamene amapereka zovala za mphepo ndi zina kwa ana omwe agonekedwa pa chipatalachi.
Iye wati thandizo lina lomwe ndi la ndalama zokwana K1million lachokera kwa anthu akufuna kwabwino.
Sabata ya mawa, Temwa akhala akugawa zovala kwa ophunzira osowa pa sukulu ya pulayimale ya Kalambo ku Area 25 mu mzinda wa Lilongwe.