Dziko la Malawi lasayinira mgwirizano ndi kampani zomwe zimapanga komanso kuyendetsa ntchito za sitima za pamadzi kuti zidzayambitse ntchitoyi pa nyanja ya Malawi.
Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, komanso nduna ya zamtengatenga, a Jacob Hara, ndi amene asayina mgwirizanowu m’malo mwa boma la Malawi.
Kampanizi zalonjeza zobwera ku Malawi posachedwa, mogwirizana ndi pempho la Dr Chakwera kuti athetse mavuto amaulendo apamadzi pa nyanja ya Malawi.
Mwambowu unachitikira munzinda wa Frankfurt m’dziko la Germany mu imodzi mwa sitima ya pamadzi zomwe amapanga m’dziko la German