Mkulu watsopano wa achinyamata m’chipani cha Malawi Congress (MCP), a Steve Baba Malondera, wapempha achinyamata ku chigwa cha mtsinje wa Shire kuti akhale ndi chidwi chopindula ndi ntchito zosiyanasiyana zimene boma likuyambitsa.
A Malondera ati panopa achinyamata a m’maboma a Chikwawa ndi Nsanje akuyenera kuyamba kuganizira njira zomwe ziwathandize kupindila ndi ntchito yaikulu ya ulimi yomwe boma likupanga mderali ya Shire Valley Transformation Programme.
“Achinyamata tiyeni tisangokhala kumadalira ena kutichitira zinthu. Kuno kuli zinthu monga za ulimi othilira zomwe zingatipindulire,” anatero a Malondera.
Iwo amayankhula pa msonkhano umene Mlembi Wamkulu watsopano wa MCP, a Richard Chimwendo Banda, akuchititsa pa sitolo zapa Nchalo ku Chikwawa.
Mkulu wa Achinyamata mu MCP-yu wapemphanso boma kuti lifewetse ndondomeko zina zotengera ngongole za NEEF. Zinthuzi nkuphatikizapo chikole chomwe chimakhalapo anthu akafuna kutenga ngongole za NEEF.
Enanso omwe ali pa msonkhanowo ndi Mneneri watsopano wa MCP, a Jessie Kabwila komanso yemwe anali Wachiwiri Oyamba kwa Spika wa Nyumba ya Malamulo, a Esther Mcheka Chitenje ndi akuluakulu ena a chipanichi.