Akuluakulu owona zaumoyo ku Blantyre ati atulutsa kumapeto a sabata ziwiri zikubwerazi zotsatira za kafukufuku wa chenicheni chomwe chinali mu mowa omwe wapha anthu okwana asanu ndi atatu mu mzindawu.
Malinga ndi mkulu wa mu office yowona zaumoyo ku Blantyre, Dr Gift Kawalazira, pakadali pano akatswiri odziwa zakafukufuku pachipatala chachikulu Cha Queens Ali mkati mounika mozama pa zinthu zomwe zinali mu mowawu.
Polankhula mu programme ya the Pot ku MBC, a Kawalazira anatinso office ya zaumoyo ku Blantyre mogwirizana ndi nthambi komanso mabungwe ena akhala akuyendera madera wosiyanasiyana pofuna kuzindikiritsa anthu zakuopsa komwa mowa wosadziwika bwinowu.
Olemba Timothy Kateta