Bungwe loona zamphamvu ndinso mafuta agalimoto m’dziko muno la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA) lachenjeza eni kampani amalo omwetsera mafuta kuti atseka malowa ngati sakutsata malamulo ogulitsira mafutawa.
Chenjezoli ladza potsatira kutsekedwa kwa malo atatu omwetsera mafuta munzinda wa Lilongwe komanso m’boma la Kasungu kaamba kogulitsa mafuta m’zigubu.
Lachiwiri, bungwe la MERA linayendera malo atatuwa ndikutseka malowo kaamba kokanika kutsata malamulo.
Malinga ndi m’modzi mwa akuluakulu ku Bungwe la MERA, a Vitumbiko Sakala, iyi ndi mbali imodzi yoonesetsa kuti aliyense akugula ndikupeza mafuta moyenera ndikupewa ngozi zamoto zodza kaamba kamafuta agalimoto.
Olemba Emmanuel Chikonso