Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

‘Ogwira ntchito za luso lamanja chepetsani utambwali’

Ogwira ntchito za luso lamanja awalimbikitsa kuti adzigwira ntchito zawo mokhulupirika  pamene akutumikira anthu m’madera mwawo.

Izi azinena ku Mangochi pamwambo opereka ma satifiketi kwa achinyamata okwana 462 omwe atsiriza maphunziro awo aluso la ntchito zamanja.

Polankhula pamwambowu, mfumu yaikulu Chowe ya m’bomali yati nthawi zambiri anthu amadandaula kuti ogwira ntchito za luso lamanja monga utelala, ukalipentala komanso zomangamanga amagwira ntchito zawo mosakhulupirika, polephera kukwaniritsa zofuna za omwe akuwatumikira munthawi yake.

“Kawirikawiri anthu amati inu anzathu matelala, inu a zomangamanga, ndinu atambwali, mumasowa chilungamo ndiye tayesetsani kuti khalidwe limeneli lithe m’madelamu,” Yatero mfumuyi.

Achinyamatawa achita maphunzirowa kudzera ku Teveta pansi pa Titukulane Project ndi thandizo lochokera ku USAID.

 

Olemba: Owen Mavula

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

School Feeding Programme retains girls in school

McDonald Chiwayula

ACB, SOS on graft-busting drill

Jeffrey Chinawa

Silver Strikers oozes confidence

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.