Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Scorchers lero imwemwetera

Atsikana amene amasewera mpira wamiyendo mu timu yadziko lino ya Scorchers adzuka ndinkhope zowala chifukwa lero boma likuyembekezeka kukwaniritsa zimene mtsogoleri wadziko lino, Dr Lazarus Chakwera, analonjeza kuti apatsidwa malo chifukwa chotenga chikho cha COSAFA m’dziko la South Africa.

Unduna wa za malo ukuyembekezeka kugawa malo kwa aliyense wa osewerawa, ndipo malowa ndi okula milingo 35 mulitali ndi milingo 25 mulifupi ku Area 45 mu mzinda wa Lilongwe.

Malinga ndi akuluakulu ku unduna wa za masewero, ntchitoyi ikuyembekezeka kuyamba mma 8:30 mmawa uno.

Related posts

K80.4 million yapezeka pamasewero a Bullets ndi Wanderers

Rabson Kondowe

Alexander ‘Cage’ Likande wamwalira

Romeo Umali

Namondwe Chido wakula mphamvu

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.