Apolisi ku Mangochi akufunafuna mayi Gladys Lingoni amene wathawa pomuganizira kuti watentha manja a mwana wake wa zaka zisanu ndi chimodzi chifukwa anadya ndiwo za soya zomwe anakonza kuti adyere msima.
Ofalitsankhani za polisi ya Mangochi, Amina Tepani, Daudi wati Lingoni ndi wammudzi mwa Sadibwa mdera la mfumu yaikulu Mkanda m’boma la Mulanje.
Panopa apolisiwo akupempha anthu akufuna kwabwino omwe angadziwe komwe mayiyo wabisala kuti awadziwitse chifukwa wasiyanso ana ena pakhomo pake.
Olemba Davie Umar.