Mfumu yayikulu Nsabwe ya m’boma la Thyolo yathokoza mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwera kaamba kogawa zitukuko m’madera onse mosayang’ana nkhope.
Mfumuyi yati mwazina, anthu a m’dera lake ndi okondwa ndi ndalama za mtukula pakhomo zomwe akulandira.
“Mudzitiyendera pafupipafupi ife mafumu ndi anthu adera lino tigwira ntchito ndi boma,” iwo anatero.
Iwo amayankhula pamene membala wamkulu wa chipani cha Malawi Congress, a Brown Mpinganjira, akuchititsa msonkhano pa Mathiya ku Thekerani m’bomalo.
Olemba : Geoffrey Chinawa