Bwalo lalikulu la milandu loona zamalamulo ku Blantyre likuyembekezeka kupereka chigamulo chake mawa ngati kuli koyenera kuti anthu ochita mchitidwe ogonanana amuna kapena akazi okhaokha adziwalola kuchita mchitidwewu mdziko muno kapena ayi.
Majaji atatu a bwaloli, Justice Joseph Chigona, Justice Chimbizgani Kacheche komanso Justice Vikochi Chima ndiwo akhala akumva mulanduwu.
Iwo akuyembekezeka kupereka chigamulochi patapita miyezi khumi atatsiriza kumva mbali zonse zokhuzidwa ndi nkhaniyi, yomwe nzika yaku Netherlands, a Wim Akster komanso a Jana Gonani aku Mangochi, amene akuti amagonana ndi amuna komanso akazi akafuna ndipo anapempha bwaloli kuti liwalore kuti adzichita mchitidwewu momasuka posintha malamulo omwe amaletsa izi.
MBC idzaulusa mulanduwu.
Olemba: Charles Chindongo