Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani Sports

Flames yagonja kaamba kosakonzeka bwino

Mphunzitsi wa timu yaikulu ya dziko lino ya Flames, Patrick Mabedi, wati timu yake yagonja ndi timu ya Burundi kaamba kakuti siinakonzekere bwino.

Mabedi wati ngakhale panali zina zomwe osewera ake achita bwino, panalinso zofooka zambiri monga kuchinyitsa zigoli zomwe zikanatha kupeweka.

“Sivuto langa kuti sitinachite bwino, timuyi ili ndi mavuto ambiri, makonzekeredwe athu sanali bwino komanso tilibe otchinga kumbuyo chakumanzere okhazikika,” anatero Mabedi.

Iye wati akudziwa kuti anthu akudandaula za kusaitanidwa kwa osewera ena akale monga Gabadinho Mhango koma wati Gaba payekha sangaphule kanthu ngati nthawi yokonzekera ingakhale yochepa.

Timu ya Malawi ikuyembekezeka kusewera ndi timu ya Burkina Faso lachiwiri ku Mali isanakumane ndi timu ya Senegal mu mpikisano omwewu.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Sambani goes AWOL again

MBC Online

Bullets appoint Chigoga as acting CEO

Romeo Umali

Zipangizo za ulimi zifika msanga — Dr Chakwera

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.