Khonsolo ya boma la Kasungu yati yakwanitsa kuzindikira anthu 23 mwa anthu 26 omwe afa pangozi, minibus yomwe anakwera itayaka moto mmudzi wa Katondo pasitolo za pa Santhe m’bomalo.
Bwanankubwa wa boma la Kasungu James Kanyangalazi wati akwanitsa kuzindikira matupiwo mothandizidwa ndi achibale. Iwo ati pakadali pano, matupiwo awatumiza ku maboma a kwawo komwe ndikuphatikizapo ku Karonga, Rumphi, Machinga ndi Chiradzulu.
Dzulo, minibus yomwe imapita ku Lilongwe kuchokera kwa Jenda, inawomba ndikupha munthu yemwe amayenda panjinga, kenako inakawomba galimoto yonyamula mafuta ya mdziko la Tanzania, isanagwire moto ndikupha anthu onse 25 omwe anali mu minibus’yo.