Khonsolo ya mzinda wa Mzuzu yati ikufuna kutolera ndalama zokwana K2.4 billion kuti igwire bwino ntchito zake zachitukuko,pansi pa ndondomeko yake ya chuma ya 2024/2025.
Mkulu wa khonsoloyi, a Gomezgani Nyasulu, amayankhula izi pokhazikitsa ntchito za chitukukozi.
“Ndalama izizi zitithandiza kuti tipange zambiri, kuphatikizapo ntchito yomanga zipinda za sukulu. Chaka chatha tinatolera ndalama yoposa 60 percent pa ndalama imene tinayerekeza,” atero a Nyasulu.
Akuluakulu ena a khonsoloyi anaonjezerapo kuti ndalamazi ziwathandizira kumalizitsa ntchito yokonza misewu komanso kuonetsetsa kuti mzinda wa Mzuzu ndi wa ukhondo.
Mfumu Thula inatsimikiza kuti imema anthu kuti adzipereka ndalama za misonkho, zotchedwa City Rates.
Olemba: Lovemore Shaba