Kefasi Chitsala waku Cobbe Barracks ku Zomba ndi yemwe wakhala katswiri wampikisano wa chaka chino wa asilikali a m’dziko muno wothamanga mtunda wa ma kilomita khumi omwe unachitikira pa bwalo la Mzuzu Golf Club.
Chitsala anathamanga mtundawu pa mphindi 31, ma second 34 komanso ma micro second 22 pomwe Nathan Chisale wochokera m’boma la Mzimba, amene si msilikali, anali wachiwiri atatha mtundawu pa mphindi 31, 48 seconds ndi 28 micro seconds ndipo Chancy Master, msilikali waku Kamuzu Barracks, anali wachitatu atathamanaga mtundawu pa 32 minutes, 13 seconds ndi 61 microseconds.
Kumaliza mtundawu pa 31 minutes 34 seconds ndi 22 micro seconds zikutathandauza kuti opikisanawa alephera kupanga mbiri yatsopano pa mpikisano othamangawu chifukwa mchaka cha 2023,pampikisano monga omwewu, omwe unachitikira pamalo omwewa, yemwe anapambana anamaliza mtundawu panthawi ya 31 minutes, 27 seconds ndi 87 micro seconds.
Asilikali amene achita bwino komanso ma barracks amene achita bwino alandira mphoto zawo.
Cholinga champikisanowu ndikupeza akatswiri amene akachite nawo mpikisano wa dziko lonse wazothamanga thamanga m’mwezi wa February chaka chino.