Timu ya Malawi ya osewera Karate yafika m’dziko kuchokera m’mayiko a Zambia ndi Zimbabwe kumene akokolola mendulo khumi ndi zisanu (15) m’mipikisano ingapo ya m’mayiko aku Africa.
Osewerawa adayamba kuonetsa chamuna m’dziko la Zambia mu mpikisano wa Lusaka Karate Open Championship pa 9 November atapambana mendulo zitatu za golide komanso zitatu za siliva ndi ziwiri za bronze.
Loweruka lapitali, anyamatawa anali m’dziko la Zimbabwe kumene anapata mendulo za golide ziwiri, za siliva zinayi komanso ya bronze imodzi mu mpikisano wa Kurai Open Championship.
Mphunzitsi wawo, a Kelvin Mwale, anati osewerawa ali ndi kuthekera kochitabwino kwambiri m’mipikisano ikuluikulu, ngati atapatsidwa zonse zofunikira pa masewerowa.
Timuyi inanyamuka m’dziko muno pa 8 November ndi osewera asanu ndi awiri kupita ku mipikisanoyi.
Masewerowa anali mbali imodzi yokonzekera mpikisano wa African Union Sports Council (AUSC) Region 5 umene ukhalepo mwezi wa June chaka cha mawa m’dziko la Namibia.