Kampani ya Nkhokwe Fertilizer Limited yapempha boma kuti liganizire zoyika feteleza wawo pa ndondomeko ya zipangizo zotsika mtengo za AIP chifukwa ali ndi kuthekera kobwezeretsa nthaka m’chimake.
M’modzi mwa akuluakulu a kampaniyi, a Fatima Sanudi, ati ali ndi chikhulupiliro kuti akatswiri amene amapanga fetereza wa Mbeya, amene amamukonza kochokera kuzinyalala, atha kupita patali ndi ntchito zaulimi boma litawathandiza.
Zaka zingapo zapitazo, boma la Malawi linavomereza kugwiritsa ntchito fetereza wa mtunduwu ndipo pakadali pano kampani zambiri m’dziko muno zikumupanga, kuphatikizapo kampani ya Nkhokwe.