Anthu omwe akukhala ku misasa ya Nyamvuwu, Matiki ndi Ngala ku Nkhotakota kaamba ka madzi osefukira m’nyanja ya Malawi ati akusowa zinthu zambiri zofunika pa moyo wawo.
A Magret Moyo omwe ndi a zaka 40 ndipo akusunga ana 7 ati anali atangomanga kumene nyumba yawo yoyamba koma pano akukanika kudyetsa anawo mokwanira ndipo akugona movutika ku misasayi ngakhale pakhomo pawo panali pa Mwanaalirenji.
A Moyo omwenso banja lawo linasokonekera kaamba kakusefukira kwa madziwa ati mpaka pano sakudziwa kuti amuna awo ali kuti.
A John Manda omwe akuyimilira bungwe la DoDMA ku Nkhotakota ati chifukwa chakuchuluka kwa anthu omwe akusungidwa ku misasayi anthuwa akukumanadi ndimavuto osiyanasiyana. Iwo apempha amabungwe ndi anthu akufuna kwabwino kuti apitirize kuthandiza anthuwa.
Olemba Yamikani Makanga