Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani

‘Mafuta akuyenera kukwera mtengo’

Komiti yoona za chilengedwe ndi kusintha kwa nyengo yauza nyumba ya malamulo kuti dziko la Malawi likuyenela ku kweza pang’ono mtengo wogulira mafuta a galimoto kuti bungwe la MERA likwanitse kutolera ndalama zofunika mu ntchito zake.

Wapampando wa komitiyi, a Welani Chilenga, ati kampani zambiri zamafuta sizikupeleka ndalama zomwe amayenela kupeleka ku bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA), zomwe akuzitcha kuti Fuel Levy m’chingerezi.

A Chilenga ati izi zikukhudzanso kwambiri kampani zoitanitsa mafuta kuchoka kunja kwa dziko lino.

Iwo ati kusapereka Fuel Levy ku kukhudza ma kampani ambiri kaamba kakuti bungwe la MERA likulephera kulipira kampani zogulitsa ndi kuyitanitsa mafuta kunja ndi kubweretsa m’dziko muno.

Kutsatira izi, aphungu a chipani chotsutsa boma cha Democratic Progressive Party anatuluka m’nyumba ya malamuloyi.

Koma, a Richard Chimwendo Banda, amene ndi mkulu wa zokambirana m’nyumbayi anauza aphungu kuti ndi koyenera kuti apitirize ku kambirana nkhaniyi ndipo kuti pa mapeto ake akuluakulu okhudzidwa ndi nkhaniyi adzachita chiganizo.

 

Print Friendly, PDF & Email

Author

  • Mayeso Chikhadzula joined MBC in 2006, he's an Investigative Journalist and Principal Reporter. He's also a News Anchor, Presenter, and producer.

Related posts

MVULA YABWERANSO

Justin Mkweu

MCP impressed with conduct of prospective contestants

Arthur Chokhotho

Over 262, 000 students sit for 2024 PSLCE exams

Arthur Chokhotho
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.