Timu ya mpira wamiyendo yadziko lino yanyamuka kupita m’dziko la Equatorial Guinea komwe akasewere ndi timu yadzikolo mumpikisano wodzigulira malo wapadziko lonse.
Timuyi ikagona ku Addis Ababa mdziko la Ethiopia ndipo idzapitiriza ulendo wawo waku Equatorial Guinea loweruka mmawa.
Timu ya Flames Ili panambala yachitatu mugulu H ndi mapointi asanu ndi imodzi.
Maulendo anayi omwe Malawi yakumana ndi Equatorial Guinea mumpikisano monga omwewu, Flames yapambana kamodzi, kufananitsa mphamvu kamodzi ndipo yagonja kawiri.