Msungichuma wa chipani cha MCP, a Albert Mbawala, alimbikitsa anthu mdera la Lilongwe Kumachenga kuti akalembetse chiphaso cha unzika pomwe kalembera wayamba m’boma la Lilongwe, kuti adzathe kuponya voti chaka cha mawa.
A Mbawala anena izi pa bwalo la sukulu ya pulayimale ya Chitipi pomwe phungu waderali, a Marko Ching’onga, amakhazikitsa chikho cha mpikisano wampira wa miyendo komanso wamanja cha ndalama zokwana K12 million mdera la mfumu Mb’watalika mderali.
A Mbawala ati izi nzofunika kwambiri popeza anthuwa adzatha kukhala ndi mwayi osankha atsogoleri omwe akuwafuna, omwenso ndi a chitukuko.
Ndipo m’mawu ake, wapampando chipani cha MCP mchigawo cha pakati, a Zebron Chilondola, ati boma lakhazikitsa ndondomeko zosiyanasiyana zotukulira dziko lino komanso anthu ake.
Iwo ati zitseko za chipani cha MCP ndizotsegula ndipo onse omwe akufuna kulowa athe kutero.
M’mawu awo atakhazikitsa chikhochi, a Ching’onga ati achita izi pofuna kuti achinyamata apeze zochita zomwe zingathandize pa moyo wawo ndi kuwapewetsa makhalidwe oyipa omwe angasokoneze miyoyo yawo.
Pamwambowu panali akulu akulu osiyanasiyana a chipani cha MCP monga nduna yoona zoti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo, a Jean Sendeza ndi ena ambiri.
#MBCDigital
#Manthu