Zonse zokhudza mwambo wachaka chino okumbukira yemwe anali katswiri wachamba cha Dancehall, Patrick Magalasi yemwe amatchuka ndi dzina loti Mafunyeta zili mchimake.
Izi zadziwika pomwe kampani ya HIFI yalengeza zopereka thandizo la zida zapamwamba zoyimbira komanso magetsi omwe akakongoletse ndikuwalitsa pamalo pomwe pakachitire mwambowu.
Mkulu owona za miyambo yazochitika ku HIFI Blessed Adam ati athandiza phwandoli poona momwe nyimbo za Mafunyeta zimasangalatsira anthu.
A Yanjanani Chigamba omwe ndiwapampando wa komiti yomwe ikuyendetsa phwandoli ayamikira HIFI komanso anthu omwe athandiza mwambowu.
Phwandoli lichitika pa 18 August chakachino ku Lilongwe ndipo alikonza ndi ndalama pafupifupi K7 miliyoni.