Mabungwe omwe siaboma ayamba msonkhano wao wamasiku awiri mu mzinda wa Harare mdziko la Zimbabwe omwe ukuunika mwadongosolo zomwe maiko a m’bungwe la SADC anagwirizana pofuna kupititsa patsogolo ntchito zosiyanasiyana zotukula maikowa kuphatikizapo ntchito zaulimi komanso zaumoyo.
Msonkhanawu ukudza patsogolo pa msonkhano omwe atsogoleri a maiko a SADC akhale nawo mu mzinda omwewu wa Harare posachedwapa.
Potsekulira msonkhanowu mkulu wa bungwe la ActionAid Zimbabwe a Joy Mabenge, anatsindika za udindo wa mabungwe omwe si aboma kuti agwirizane kuti zokambirana zawo zikhale zolumikizana ndi mutu wa msonkhano wa atsogoleri a maiko a m’bungwe la SADC omwe ukulimbikitsa ntchito za luso zomwe zingatsekule makomo achitukuko pounikira dongosolo lotukula ntchito zamafakitale.
“Kukambitsirana kwathu, amayi ndi abambo, ndikulimbitsa udindo wa mabungwe omwe siaboma kuti alimbikitse kalondolondo wantchito zosiyanasiyana zotukula maiko a m’bungwe la SADC maaka pounikila ntchito, zamafakitale komanso zaulimi,” anatero a Mabenga.
A Julie Middleton, omwe amayang’anila ntchito yolimbikitsa kalondolondo mmaiko a SADC komanso mgwirizano pantchito m’maikowa ati pali chiyembekezero kuti zambiri zomwe maikowa anasayinira ziyamba kuchitika monga kukhala ndi malamulo ofanana komanso kukhala ndi Nyumba ya Malamulo ya maiko a m’bungweli.
M’mawu ake mkulu wa bungwe loona zaumoyo la Malawi Health Equity Network, a George Jobe, yemwenso ndi nthumwi pa msonkhanowu, ati msonkhanowu uli ndi cholinga chozamitsa mgwirizano m’madera osiyanasiyana monga zaumoyo.
“Tikuyang’ana kwambiri m’magawo angapo monga zaulimi ndi zaumoyo. Komanso tikuunika mwachidwi zomwe sitinakwanilitse koma zomwe tikufuna kukwaniritsa ngati bungwe la SADC, ndi zomwe maboma athu achite pokwaniritsa mapangano a mayikowa.
“Tagawana zomwe dziko la Malawi lachita pa mgwirizano omwe unachitika ku Abuja mdziko la Nigeria (Abuja Declaration) omwe umato 15 peresenti ya bajeti ya dziko iyenera kuperekedwa ku ntchito zaumoyo. Takambilananso momwe matenda a Edzi akhudzira achinyamata ndi zomwe maiko a mu SADC akuyenera kuchita pofuna kulimbikitsa uchembere wabwino komanso kupewa matenda pakati pawo,” anatero Jobe.
Pamapeto pa mnsonkhanowu, amanga mfundo zomwe atsogoleri a maiko a mu SADC akuyenera kudzakambirana pamsonkhano wawo ndikuvomereza masiku akubwerawa.