Apolisi mchigawo chakumpoto agwira anthu asanu ndi m’modzi m’boma la Kasungu powaganizira kuti ndiwo anaba lamya za m’manja zokwana makumi asanu (50) kumwambo wazoyimba-yimba wa Yo Maps omwe unachitikira mumzinda wa Mzuzu.
Mneneri wapolisi mchigawo cha kumpoto a Maurice Chapola wati anthuwa anagwidwa pamalo ochitira chipikisheni m’boma la Kasungu pamene apolisi anadabwa kuti anthuwa amakanika kuyankha mafoni amene amalira nthawiyo.
A Chapola atsimikiza kuti anthuwa ndiochokera mu Mzinda wa Lilongwe ndipo anabwera ku Mzuzu kudzachita upandu.
Mneneriyu anathokozanso apolisi aku Kasungu pogwira ntchito yotamandika yomanga oganiziridwawa.
A Chapola achenjezanso anthu omwe amakonza zochitika zosiyanasiyana zimene zimakopa anthu ochuluka kuti adzigwira ntchito limodzi ndi apolisi pothandiza kusungitsa bata ndi mtendere kaamba kakuti opalamula amachita mantha ndi apolisi chimene chili chiletso kwa ofuna kupalamula milandu.
Wolemba: Joel Nkhata