Nduna ya zokopa alendo, a Vera Kamtukule, ati nthawi yakwana kuti a Malawi adzipindula ndi zachikhalidwe cha chi Malawi poganiza mwakuya pa m’mene angakopere alendo pogwiritsa ntchito masamba a mchezo monga Facebook, TikTok komanso Instagram, mwa zina.
A Kamtukule amayankhula izi atayendera mudzi wa chikhalidwe wa Gwirize, kwa Mfumu yaikulu Pemba m’boma la Salima umene unawachititsa chidwi chifukwa ukupititsa patsogolo mbiri yake kudzera pa masamba a mchezowo.
Mudziwu udakhazikitsa malo ochitira magule komanso kulandilira alendo. M’mbuyomu, udapatsidwa mphoto ya pafupifupi K2 million mu mpikisano wachikhalidwe.
Ndunayi yati ndi kofunika kuti midzi ina itengerepo chitsanzo, ponena kuti muchikhalidwe muli chuma ngati chitasamalidwa ndi kugulitsidwa kwa alendo kudzera munjira zamakonozi.
Wapampando wa mudziwu, a Noah Chana, anapempha boma kuti lithandizire ndi misewu yamakono yopita kumudziwu chifukwa anati akumanga nyumba yogulitsa chakudya komanso yodyeramo yomwe mudzipezeka zakudya zachiMalawi komanso malo osungirako mbiri ya dziko lino.