Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

SINDIKUONA TSOGOLO KU CHIPANI CHA DPP – CHAMBO

Phungu wadera la Mangochi-Makanjira a Benedicto Chambo ati iwo ndi anthu amdera lao lomwe ndi kumpoto kwa boma la Mangochi alipambuyo pa boma la Malawi Congress Party ndi mtsogoleli wake Dr Lazarus Chakwera.

Poyankhula pomaliza mpikisano wa chikho cha K1.5 miliyoni  Thembachako Final Bonanza pabwalo la Dzenza ku Area 25 mu mzinda wa Lilongwe  a Chambo ati zomwe zikuchitika mdziko muno pa chitukuko ndi zachilendo. Iwo ati Prezidenti Chakwera sakusankha dera popereka chitukuko.

“Tiyeni tiunike zitukuko zomwe boma la a Chakwera lachita mkanthawi kochepaka, ndi okhawo amaganizo woipa omwe sakuona,” anatelo a Chambo.

Iwo ati zina zomwe zawapangitsa kusintha chikwangwani ndi kusagwilizana komwe kwakula mchipani cha Democratic Progressive -DPP. Mwa zina a Chambo ati sakuona tsogolo ku chipani cha DPP.

Iwo ati akukonza zopanga chisankho choima pa tiketi ya DPP, paokha kapenanso chipani cha MCP pa chisankho cha 2025.

Pamwambowu panalinso akuluakulu wosiyanasiyana kuphatikizapo mkulu woona za achinyamata ku chipani cha MCP yemwenso ndi nduna yamaboma ang’ono a Richard Chimwendo Banda.

#mbcmw
#mbcnewslive
#mbconlineservices

Print Friendly, PDF & Email

Author

  • Mayeso Chikhadzula joined MBC in 2006, he's an Investigative Journalist and Principal Reporter. He's also a News Anchor, Presenter, and producer.

Related posts

A Nankhumwa akana kulankhula mawu omaliza potsekera msonkhano wa aphungu

Olive Phiri

Sitima ina yonyamula mafuta iyamba kuyenda sabata ya mawa

Beatrice Mwape

M’busa wapereka mimba kwa mtsikana atamunamiza kuti amuchiritsa matenda

Charles Pensulo
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.