Banki ya National yapanga phindu lokwana K42.1 billion mu miyezi yapakati pa January mpaka June chaka chino.
Izi ndi malinga ndi kalata yazachuma yomwe bankiyi yatulutsa ndipo yasayinidwa ndi mkulu wa bankiyi a Harold Jiya komanso wapampando wake a Jimmy Lipunga mwa ena.
Phinduli ndilokwera ndi ma peresenti 19 poyerekeza ndi K35.5 billion yomwe bankiyi inapeza nthawi ngati yomweyi chaka chatha.
Kalatayi yati phinduli lapezeka kaamba koti ndalama zomwe makasitomala anasungitsa zinachuluka zomwe zapangitsa kuti anthu akongole zambiri.
Banki ya National ndi imodzi mwa banki zomwe ziri pa msika wamasheya wa Malawi Stock Exchange.