Boma lati ndilokhumudwa ndi momwe ntchito yomanga msewu ochokera ku Chitipa kupita ku Ilomba ikuchedwera kufika kumapeto.
Nduna yoona za mtengatenga, a Jacob Hara, ndiwo anena izi ku Chitipa atayendera ntchito yomanga msewuwu.
Iwo ati boma linapereka ntchitoyi kwa kampani za m’dziko mom’muno koma ati ndiokhumudwa ndimomwe kampanizi zikuchedwetsera ntchitoyi.
“Momwe taonera ntchitoyi, taganiza zobweretsa makampani ena kuti athandize makampani omwe ali kunowa kuti ntchitoyi ithe msanga,” anatero a Hara.
Mfumu Mwawulambya ya m’bomali yati ili ndichikhulupiliro kuti tsopano ntchitoyi iyamba kuyenda bwino, potengera ndi zomwe ndunayi yanena.
Msewu wa Chitipa Ilomba ndiotalika makilomita 30.
Wolemba: Henry Haukeya