Mkulu oyang’anira ndende za m’dziko muno, a Masauko Ng’ombeyagwada Wisikoti, ati kundende ndi malo othandiza kusintha khalidwe la munthu osati malo ongokhaulitsira iwo ophwanya malamulo.
A Wisikoti amafotokoza izi pamene bungwe la Uthunthu limakhazikitsa m’gwirizano ndi bungwe la TEVETA kuti lidziphunzitsa achinyamata a ndende za m’dziko muno maphunziro ambiri kuti akadzakhala mfulu asadzasowe poyambira.
Bungwe la Uthunthu ndi la chikhristu ndipo limathandiza anthu kukhala odzidalira paokha kudzera m’maphunziro a ntchito zamanja.
Mkulu wa bungweli, a Caswel Mkanda, ati agwiritsa ndalama zokwana K100 million zomwe anasonkha ndi mamembala awo ndipo anamema anthu akufuna kwabwino kuti awathandize kupitiliza zimene ayambazi.
Poyankhulapo, mkulu wa bungwe la TEVETA, a Elwin Chiwembu-Sichiola, ati maphunziro amenewa akayambira ku ndende za Maula ndi Kachere mu Mzinda wa Lilongwe.
A Sichiola ayamikira bungwe la Uthunthu ndipo ati apitiliza kugwira nalo ntchito limodzi.