Bwalo la milandu m’boma la Mangochi lalamula a Alice Mailosi azaka 31 kuti akagwire ukayidi wakalavula gaga kwa zaka ziwiri chifukwa chovulaza mamuna wawo, yemwe sanatchulidwe dzina, pomuthira madzi owira atasemphana pankhani zachikondi.
Oweruza milandu, a Muhammad Chande, anapereka chilangochi kuti ena atengerepo phunziro.
Ofalitsa nkhani pa Polisi ya Mangochi, a Amina Tepani Daudi, ati mlanduwu unachitika pa 8 March chaka chino pamene a Mailosi amaganizira kuti mamuna wawo amakumanabe ndi bwenzi lawo lakale yemwe dzina lake ndi Alice Ida wa zaka 21.