Khansala wapampando watsopano m’dera la Mwasa ku Mangochi, a Stewart Mwase, alonjeza kuti alimbikitsa ntchito zachitukuko zomwe anaziyamba kale pa nthawi yomwe asanasankhidwe pa udindowu.
A Mwase amalankhula izi pamwambo owalumbilitsa omwe umachitika m’boma la Mangochi m’mawawu.
Iwo anapambana pa chisankho chapadera pa 23 July chaka chino ndipo anayimira chipani cha Malawi Congress (MCP).
“Ndathandizapo ntchito yomanga mijigo, mizikiti, ndi zina zambiri, ndipo pakadali pano chidwi changa chili pomanga chipatala chaching’ono chomwe chidzithandiza anthu amdera langa,” iwo anatero.
Pachisankho chapadera chosankha khansala wadera la Mwasa m’boma la Mangochi, a Stewart Mwase, anapambana atapeza mavote 1073.
Olemba Owen Mavula