Khonsolo ya mnzinda wa Zomba yasankha a Christopher Jana adera la Mpira ngati mfumu yatsopano ya mnzindawu.
A Jana alowa mmalo mwa a Davie Maunde omwe akhala pa mpandowu kuchoka chaka cha 2021 atasankhidwa mmwezi wa December mchakacho.
A Anthony Gonani ndiye wachiwiri kulowa mmalo mwa a Munira Bakali a Likangala ward.
A Jana anakhalaponso pa udindowu mchaka cha 2018 kufika 2020 pomwe khansala Benson Bula anatenga udindowu kufikira 2021.