Masana ano bwalo la Magistrate mnzinda wa Lilongwe likuyembezeka kupereka chigamulo pa pempho labelo lomwe oyimira a Chiyanjano Mbedza anapereka sabata yatha.
A Mbedza anawamanga pa 22 July chaka chino powaganizira kuti ndi amene amajambula ndi kufalitsa uthenga odzetsa chisokonezo pa makina a intaneti pa tsamba lake lotchedwa Bakili Muluzi TV.
Mwa zina, ati iwo amaloza zala anthu ena kuti akukhudzidwa ndi imfa ya yemwe anali wa chiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino malemu Dr Saulos Chilima.
Lachisanu lapitalo, bwaloli linakana kupereka belo kwa a Mbedza pofuna kupereka mpata kwa apolisi kuti amalize kafukufuku wawo.