Khonsolo ya mnzinda wa Lilongwe usiku uno ikugwira ntchito yosesa komanso kuchotsa zinyalala mu munzindawu.
Mfumu yamnzindawu, a Esther Sagawa, ndiyo ikutsogolera ntchitoyi yomwe yayambira ku City Centre.
Malinga ndi a Sagawa, adzigwira ntchitoyi usiku pofuna kuonetsetsa kuti ikuchitika moyenera ndipo ati azichita izi katatu pasabata iliyonse.
Iwo apempha eni ma shop munzindawu kuti akhale ndi motaila zinyalala ndicholinga choti ntchito yokonza mumnzindawu isamavute.