A Kondwani Nyasulu awasankha kukhala mfumu ya mnzinda wa Mzuzu pazisankho zomwe zikuchitika mu mzindawu zosankha mfumuyi komanso wachiwiri wake.
A Nyasulu, amene ndi a chipani cha UTM, awasankha atapeza mavoti asanu ndi anayi pomwe a Desire Nyirenda a MCP apeza mavoti asanu ndi awiri.
Anthu omwe akuponya votiyi alipo 16.
Zisankhozi anayamba aziyimitsa kamba koti khansala Pillie Chiumia wadera la kuzambwe kwa Mchengautuba mu mzindawu anadandaula kuti a Nyirenda si oyenera kuima nawo kamba koti akuyankha mlandu ku khoti woganiziridwa kuti anagonana ndi mwana wachichepere.
Izi zinatengera akulu akulu akhonsolo komanso odziwa zamalamulo kuunika dandauloli ndipo atakambilana mukanyumba kamata, anagwirizana kuti a Nyirenda ndi oyonera kuima chifukwa khoti silinagamule mlanduwu.
Panopa zisankho zikupitilirabe kusankha wachiwiri kwa meya wa mzindawu.