Mtsikana wazaka 15, Eneles Namusanyo, yemwe anali sitandade 5, wadzipha pokwiya chifukwa chodzudzulidwa khalidwe la zibwenzi.
Ofalitsankhani zapolisi ku Mulanje, Innocent Moses, wati mtsikanayo anali pachibwenzi ndi mnyamata wina ndipo mayi ake atadziwa izi, anakhala naye pansi kumulangiza kuti asamachite khalidweli.Kenako mayiwo anachoka pakhomopo ndipo pobwera sanamupeze mwana wawoyo mpaka tsiku lotsatira.
Kutacha, anthu anamupeza atadzimangilira ku denga la nyumba yawo.
Malemuyu anali wa mmudzi wa Ngongondole, mfumu yaikulu Mabuka m’boma la Mulanje.