Akuluakulu a ofesi ya zaumoyo ku khonsolo ya boma la Balaka awayamikira polimbikitsa ntchito yoonetsetsa kuti anthu akulandila thandizo la zachipatala mosavuta.
Nduna ya za umoyo a Khumbize Chiponda amalankhula izi m’bomali, pomwe amatsegulira zipinda zatsopano zosamalira odwala zomwe khonsoloyi yamanga pachipatala chachikulu chaboma.
Ntchitoyi aigwira pogwilitsa ntchito zina mwa ndalama zochokera kuthumba lapadera lomwe makhonsolo akulandila kuchokera ku boma kuti zithandizile kukonza komanso kumanga malo othandizila ntchito za umoyo.
Mwa zina, khonsoloyi ikumanganso chipatala chochilira amai oyembekezela kwa chiyenda usiku, pofuna kuchepetsa ulendo omwe amaiwa amayenda kuti akapeze thandizo ku chipatala chachikulu.
Wolemba: Owen Mavula