Flames ya osewera akale idzasewera ndi timu ya osewera akale a m’dziko la Zambia mwezi wa mawa m’dziko muno.
Membala wa board ya bungwe la osewera akalewa la Football Legends Association, a Rashid Ntelera, wati padakali pano akukonzekera masewerowo kuti adzakhale apamwamba ndi achikoka.
Awa adzakhala masewero achibwereza chifukwa Malawi inagonja ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi mu masewero oyamba ku Zambia chaka chatha.
Clifford Mulenga komanso Ignicious Lwipa anamwetsa zigoli za Zambia pamene Jimmy Zakazaka ndi amene anagoletsera Malawi.
Bungwe la Football Legends Association, lomwe anayambitsa ndi a Jim Kalua, linabweretsa pamodzi osewera komanso oyendetsa mpira akale ndipo pakadali pano lili ndi mamembala opitilira 124.
Olemba: Amin Mussa