Mtsogoleri wa Kabaza Association of Malawi (KAMA), a Joseph Petulo, wapempha mamembala awo amene ndi akabaza oposa 3.8 million, kuti apatule nthawi yawo ndi kupeza mpata okalembetsa m’kaundula wa voti.
Iwo ayankhula izi pomwe gawo lachitatu lakalemberayu likupita kumapeto.
“Nthawi zina akabaza ambiri amagwira ntchito kuyamba m’mawa mpaka mdima. Siyani njingayo kaye kalembetseni,” a Petulo anatero.
Iwo anachenjezanso akabaza kuti asamamwe bibida pantchito komanso adzipewa kutenga anthu okayikitsa ndi kuyenda usiku.
“Wakufa savota, utha kukalembetsa koma kufa chifukwa changozi zopeweka, tisamale munyengo yakhirisimisiyi ndi nyuwere,” iwo anatero.
Gawo lachitatu lakalembera linayamba pa 28 November chakachino ndipo litha pa 11 December chakachino.