Malawi Broadcasting Corporation
Crime Local Local Nkhani

A Chisale akuyankha mulandu

Bwalo la Magistrate ku Lilongwe lili mkati momva mlandu wa a Norman Chisale yemwe anali wachitetezo wa mtsogoleri opuma wa dziko lino, Professor Arthur Peter Mutharika.

Bwaloli likumva kuchokera kwa mboni zitatu za boma zomwe ndi wachitetezo wa wachiwiri kwa mkulu wa ACB, Sergeant Enerst Chimanga, yemwe anali mkulu ozenga milandu, a Steven Kayuni, komaso wachiwiri kwa mkulu wa bungwe la ACB, a Hillary Chilomba.

Bwaloli layamba kumva mboni ya chisanu ndi chitatu Sergeant Enerst Chimanga omwe afotokoza kuti anakumana ndi a Chisale ku office ya ACB ku Lilongwe pomwe a Chisale anabwera kuti azafunsidwe mafunso. A chimanga ati anamva mawu a Chisale akuyakhula ndi wachiwiri kwa mkulu wa bungwe la ACB. Iwo ati a Chisale anayakhula mawu oti “a MCP komaso mkulu ozenga milandu mukundilakwira, ndimafuna ndikumane ndi mkulu wa bungwe la ACB koma ali ndi mwayi kuti palibepo, tsiku lina ndikadzabwera padzalira mfuti komaso mabomba pano.”

Padakali pano bwaloli likumva umboni wa a Chilomba omwe ndi wachiwiri kwa mkulu wa bungwe la ACB.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

JB touts Mega farms as game changer

Simeon Boyce

MARANATHA FALLS VICTIM TO FAKE NEWS

McDonald Chiwayula

President Chakwera to open Agriculture Investment Conference

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.