Mkulu oyang’anira zomangamanga ku unduna wa zaumoyo, Dr Sanderson Kuyeli, wati gawo loyamba pantchito yomanga chipatala cha Mponela Community m’boma la Dowa latsala pang’ono kutha.
Iwo ayankhula izi atayendera chipatalachi pamodzi ndi adindo amu ofesi ya mtsogoleri wa dziko lino ndi maunduna.
Chipatala cha Mponela Community chikuyembekezeka kuchepetsa kuchulukana kwa anthu ofuna thandizo pa chipatala cha boma ku Dowa.
Chipatalachi chikhala ndi zipinda zochita opaleshoni, zipinda zogona anthu odwala momwe mukhale makama 100, nyumba za anthu ogwila ntchito okwana 46 komanso nyumba yachisoni, ndi zina zambiri.
“Malo ano pamene pali chipatala chino tikukhulupilira kuti chikatha chidzathandiza ngakhale anthu achita ngozi mu msewu wa M1, umene panopa boma likukonzanso,” Dr Kuyeli anatero.
Iwo anawonjezeranso kuti unduna wawo ukukonza zomalizitsa zipatala zimene ntchito yomanga idayamba yayima monga chipatala cha Chikapa ku Machinjiri munzinda wa Blantyre.