Ofalitsa nkhani ku chipani cha Malawi Congress (MCP), a Jessie Kabwila, ati chipani chotsutsa cha DPP chidanena bodza ku msonkhano wawo waukulu pamene adati m’dziko muno simukuchitika chitukuko pansi pa mtsogoleri wa dziko la Malawi, Dr Lazarus Chakwera.
A Kabwila amayankhula izi atayendera ntchito zachitukuko zomwe zili mu mzinda wa Blantyre.
Zina mwa ntchitozi ndi yomanga malo okwelera mabasi ku Mibawa, yomanga msewu ku Lunzu, msewu opita ku Machinjiri kuchoka msewu wa Magalasi, mlatho watsopano wa Makalanga ku Machinjiri ndi msewu olumikiza Makhetha ndi Ndirande.
Iwo anati ndi zokondweretsa kuona ntchito za chitukuko zikuperekanso mwayi wa ntchito kwa a Malawi.
A Kabwila aperekanso chitsanzo cha ntchito zobwezeretsa njanji ngati zina mwa zitukuko zomwe boma lidakhazikitsa.