Chipatala cha South Lunzu m’boma la Blantyre chakonza ulendo wa ndawala mwezi wa mawa pofuna kupeza thandizo la ndalama zokwana K70 million zimene akufuna kuti agwiritse ntchito pokonza mavuto ambiri amene ali pa chipatalachi.
Wapampando wa komiti imene imayang’anira chipatalachi, a James Kalungwe, wati ndalamazi azigwiritsa ntchito pomanganso mpanda umene unagwa ndi namondwe Freddy komanso kukonza zimbudzi zimene zipangizo zake zinabedwa.
A Kalungwe anaonjezeranso kuti akufuna agwiritse ntchito ndalamazi pokhala ndi malo abwino otayira zinyalala komanso malo okhala odikilira odwala ndi kugula zitseko ndi mipando.
M’modzi mwa mzika za kuderali, amenenso ndi olembankhani, Deus Sandram, anati ndi okhudzidwa ndi momwe zithu zilili pa chipatalachi ndipo walonjeza kuthandizira kuti chipatalachi chipeze thandizo la ndalamazi.