Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Chakwera ayamikira dziko la Mozambique

Mtsogoleri wa dziko la Malawi wayamikira boma la Mozambique kaamba ka ubale wabwino omwe ulipo panopa umene wachititsa kuti dzikolo lipereke malo ku Nacala oti boma la Malawi likhale ndi malo oti lidzilandilirapo katundu.

Dr Lazarus Chakwera amanena izi mu mzinda wa Frankfurt m’dziko la Germany komwe akukambilana ndi makampani opanga komanso kuyendetsa sitima zapamadzi.

Dr Chakwera ati makampaniwa atengelepo mwayi wa ubale wa dziko la Malawi ndi maiko oyandikana nawo kuphatikizapo Zambia kuti akhonza kuyambitsa maulendo a pamadzi othandiza aMalawi panyanja pothana ndi mavuto odalila sitima imodzi ya Ilala.

Dr Chakwera ati panyanja ya Malawi pakakhala sitima zingapo, anthu samavutikanso kudikila nthawi yaitali kuti sitima ina ibwele zomwe zidzathandize kutukula miyoyo ya anthu odalila sitima zapamadzi monga ku Likoma ndi maboma a m’mphepete mwa nyanja ya Malawi.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Akakhala ku ndende zaka 19 chifukwa chovulaza mkazi wake wakale

Charles Pensulo

Engineer Mumba, Zikhale athandiza Chakwera

MBC Online

Prezidenti Chakwera ndi wa masomphenya — Mkaka

Mayeso Chikhadzula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.