Mbadwa zokhudzika zati zifukwa za gulu la Malawi First lomwe limatsogoleredwa ndi a Bon Kalindo zoti achitire zionetsero ndi zosamveka ndipo apempha a Malawi kuti asatenge nao mbali.
Poyankhula ndi atolankhani mu mnzinda wa Lilongwe magulu oposa asanu monga Mbadwa Zokhudzika, Tigwirane Mmanja , Human Rights Ambassadors, Child Rights Advocacy komanso Citizen Advancement for Economic Revolution ati iwo akugwirizana ndi bungwe la Malawi Revenue Authority kuti liziika chizindikiro cha msonkho (tax stamps) pakatundu obwera mdziko muno poti izi zithandiza kuti mchitidwe ozembetsa katundu uthe.
Mneneri wa bungwe la Child Rights Advocacy and Paralegal Aid Centre, a Agape Khombe ati akudabwa kuti a Màlawi First akufuna kudzachita zionetsero pa 8 August tsiku lomwe chipani cha MCP chikudzachititsa msonkhano wake waukulu zomwe zitha kudzadzetsa chisokonezo.
Mabungwewo atinso zomwe a Malawi First akunena kuti bungwe la National Registration Bureau likulembetsa ana osakwana zaka 16 sizoona.