Boma lapempha anthu ochita ndale m’dziko muno kuti asamalowelere ntchito za ma khonsolo ndi cholinga chofuna ku kwaniritsa zolinga zawo pa ndale.
Nduna ya za maboma a ang’ono, a Richard Chimwendo Banda, ndi amene ananena izi mu mzinda wa Blantyre pamkumano wa masiku awiri womwe adindo a m’ma khonsolo a m’chigawo cha kumwera amafotokoza momwe agwilira ntchito zawo kwa miyezi ingapo yapitayo.
Ndunayi inapemphanso atsogoleri m’ma khonsolowo kuti azigwira ntchito zotumikira anthu omwe ndi osowa.
A Chimwendo Banda anatinso m’chitidwe wosokoneza ntchito za chitukuko m’ma khonsolo umakula maka pamene dziko likuyandikira kuchita chisankho.
“Musalole kuti ntchito zachitukuko ziime chifukwa chofuna kusangalatsa anthu ena a ndale, ” a Chimwendo Banda anatero.
Pamkumanowu, kunali a bwanankubwa, oyang’anira ntchito za chuma m’ma khonsolo, aphungu akunyumba yamalamulo komanso ma khansala a m’chigawo cha kum’mwera mwa ena.