Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Chikakula patuka, Ramadhan watumiza ‘leka’

Mphunzitsi wamkulu wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Nsazurwimo Ramadhan, wati watula pansi udindowu kutsatira kugonja kwa timuyi mumasewero awiri motsatizana mu TNM Super League.

Ramadhan, yemwe adalonjeza kubweretsa chimwemwe kubanja la Manoma, waona ngati kumaloto atagonja ndi timu ya Mzuzu City Hammers ndi zigoli ziwiri kwa duu loweruka patangopita masiku ochepa timuyi itagonjaso ndi timu ya Silver Strikers ndi zigolinso ziwiri kwa duu.

Ramadhan, popereka kalata yotula pansi kwa mtsogoleri wa timuyi Thom Mpinganjira, wati sakufuna kukakamiza zinthu.

“Ngati tebulo silikufuna kukupatsa chakudya kulibwino kuzisiya,” iye watero.

Timu ya Wanderers ili ndi mapointi khumi ndi awiri pamndandanda wa matimu omwe akusewera mu ligi yaikuluyi ndipo ikusiyana ndi mapointi khumi ndi timu yomwe ikutsogola ya Silver Strikers ndipo onse asewera masewero okwana asanu ndi atatu.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Blue Eagles yatsala ndi ma poyinsi atatu kuti ibwerere mu super league

Foster Maulidi

UK yathandiza Lake of Stars ndi K169 Miliyoni

Emmanuel Chikonso

Save The Children yapereka mbaula zamakono ku Lilongwe

Lonjezo Msodoka
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.