Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

Boma latsindikanso kuti palibe afe ndi njala

Mlembi wamkulu wa chipani cha Malawi Congress (MCP), a Richard Chimwendo Banda, wabwerezanso kunena kuti palibe amene atafe ndi njala chifukwa boma likugawa chakudya kwa mabanja amene ali ndi vuto la njala.

A Chimwendo Banda anena izi ku Kasinje m’boma la Ntcheu pamsonkhano umene iwo pamodzi ndi akuluakulu ena achipanichi anachititsa.

“Tikudziwa kuti anthu akuvutika, koma anthu asade nkhawa chifukwa chimanga chikugawidwa. Kuno tibweretsako matumba 1,000 m’masiku angapo akudzawa,” a Chimwendo Banda anatero.

Pa nkhani zachitukuko, a Chimwendo Banda, amenenso ndi nduna yaza maboma ang’ono, anati boma la Prezidenti Dr Lazarus Chakwera lagwira ntchito zambiri zachitukuko zolimba zimene maboma apitawa amazinyalanyaza.

Iwo anatchulapo ntchito monga yokonza misewu m’mizinda ndi m’matauni, kumanga midadada 11,000 yophunziliramo, kuonjezera chiwerengero cha ophunzira aku sukulu zaukachenjede omwe amathandizidwa ndi boma kuchoka pa ophunzira 10,000 kufika pa 30,000, kukonzanso njanji ndi zitukuko zina zambiri.

A Chimwendo Banda anati Prezidenti Chakwera adzapambana pa chisankho cha chaka cha mawa.

Kwa achinyamata, a Chimwendo Banda anawalangiza kuti alimbikitse bata ndi mtendere osati kugwiritsidwa ntchito pochita zipolowe.

Phungu wadera la kumpoto kwa Bwanje m’boma la Ntcheu, a Nancy Chaola Mdooko, komanso mfumu yaikulu Ganya anayamikira boma kaamba ka ntchito zachitukuko m’dera lawo monga magetsi a mphamvu ya dzuwa. Komabe, iwo anapempha boma kuti likuze chipatala cha Kasinje.

Olemba: Isaac Jali

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Rumphi shines in NEEF loans repayment

MBC Online

Expect heavy rains — MET

MBC Online

M’busa apempha anthu kuti athandize osowa

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.